بِفَاطِمَةْ قَدْ صَفَا حَالِي
Ndi Fatima, mkhalidwe wanga wayeretsedwa
Ny
بِفَاطِمَةْ قَدْ صَفَا حَالِي وَنِلْتُ الْمَرَامْ
بِضْعَة مُحَمَّدْ حَبِيبِ اللهْ خَيْرِ الْأَنَامْ
Chifukwa cha Fatima mkhalidwe wanga wayeretsedwa ndipo ndapeza zonse ndimafuna
Mbali ya Muhammad, Wokondedwa wa Allah, wopambana mwa anthu onse
أَعْلَى لَهَا اللهْ قَدْراً فِي الْعُلَا وَالْمَقَامْ
نِعْمَ الْبَتُولْ الْرَّضِيَّةْ نُورْ كُلِّ الْظَّلَامْ
Allah anakweza udindo ndi malo ake kukhala apamwamba kwambiri
Ndi wabwino kwambiri Msungwana Woyera, Wovomerezeka, kuunika mu mdima uliwonse
أُمِّ الْحَسَنْ وَالْحُسَيْنْ أَهْلِ الْمَرْقَى الْعِظَامْ
لَهُمْ عَطَايَا مِنَ الْمَوْلَى كِبَارٌ جِسَامْ
Amayi a al-Hasan ndi al-Husayn, a kukwera kwauzimu kwakukulu
Olandira mphatso zazikulu ndi zolemekezeka zochokera kwa Mulungu
هُمْ سَادَةَ أَهْلِ الْجِنَانِ الْعَالِيَةْ يَا غُلَامْ
مَنْ حَبَّهُمْ صِدِقْ بَا يِسْكُنْ بِدَارِ الْسَّلَامْ
Iwo ndi atsogoleri a m’minda ya Edeni ya m’mwamba, inu mnyamata
Aliyense wowakonda moona mtima adzakhala m’nyumba ya mtendere
وَمَنْ تَعَلَّقْ بِهِمْ يَظْفَرْ بِنَيْلِ الْمَرَامْ
أَكْرَمْتِ يَا بِضْعَةَ أَحْمَدْ فَانْعَمِي بِالْتَّمَامْ
Ndipo amene adziphatika kwa iwo adzapeza zokhumba zonse
Muli wowolowa manja kwambiri, inu mbali ya Ahmed, choncho malizitsani chisomocho
وَامْنَحِي عَبْدَكُمْ فِي الْقُرْبْ أَعْلَى وِسَامْ
نَقُومْ بِحَمِلْ الْرَّيَاتِ الْهُدَ أَحْسَنْ قِيَامْ
Ndipo patsani kapolo wanu ulemu waukulu wa kukhala pafupi nanu
Tipitirize kunyamula mbendera za chiongoko m’njira yabwino kwambiri
تَعُمْ دَعْوَتُهْ فِي الْأَكْوَانْ كُلِّ الْأَنَامْ
نِلْبَسْ خِلَعْ إِرْثْ مَا يَصِفْ سَنَاهَا كَلَامْ
Kuti kuitana kwake kufikire zolengedwa zonse m’chilengedwe
Tivalidwe mwinjiro wa choloŵa chimene kuwala kwake n’kosalongosoleka
يَا نُورْ قَلْبِي وَيَا أُمِّي عَلَيْكِ الْسَّلَامْ
فِي كُلِّ حَالٍ وَشَأْنٍ كُلِّ لَحْظَةْ دَوَامْ
Inu kuunika kwa mtima wanga, inu amayi anga, mtendere ukhale pa inu
Nthawi zonse, mu mkhalidwe uliwonse ndi pa chilichonse
عَلَيْكِ صَلَّى إِلَهِي مَعَ أَبِيكِ الْإِمَامْ
إِمَامْ كُلِّ الْوَرَى فِي كُلِّ خَاصٍّ وَعَامْ
Allah akudalitseni pamodzi ndi atate anu, Imamu
Mtsogoleri wa zolengedwa zonse, akuluakulu ndi anthu wamba
الْشَّافِعِ الْمُبْتَغَ يَوْمَ الْلِّقَاءْ وَالْزَّهَامْ
يَوْمِ الْمَلَائِكْ تُنَادِي جَمِعْ كُلِّ الْأَنَامْ
Mkhalapakati wofunidwa pa tsiku la kukumana ndi la chigulu
Tsiku limene angelo adzaitana msonkhano wa anthu onse
غُضُّوا أَبْصَارَكُمْ تَمُرْ بِنْتِ الْنَّبِيِ بِالْسَّلَامْ
وَنَكِّسُوا رُؤُوسَكُمْ مَا أَعْظَمَهْ وَاللهْ مَقَامْ
“Chepetsani maso anu pamene mwana wa Mneneri akudutsa mu mtendere
Weramisani mitu yanu” Ha! Uli udindo waukulu bwanji pamaso pa Allah!
تِذَكَرِينِي مَعَكِ أَعْبُرْ وَمَنْ لَهُ ذِمَامْ
حَاشَاكِ يَا أُمَّنَا تِنْسِينْ هَذَا الْغُلَامْ
Ndikumbukireni, kuti ndidutse nanu pamodzi ndi chisamaliro chanu
Sizingatheke kwa inu, amayi, kuiwala mnyamata wanuyu!
مَحْسُوبَكُمْ يَرْتَجِيهْ مِنْكُمْ بِهِ الْإِهْتِمَامْ
أَنْتُمْ مَرَامُهْ وَمَقْصُودُهْ وَنِعْمَ الْمَرَامْ
Wotsatira wanu akuyembekezera chidwi chanu
Inu ndinu cholinga ndi chokhumba chake, ndipo ndi chokhumba chabwino bwanji!
يَا بِنْتَ طه فُؤَادِي فِي مَحَبَّتِكْ هَامْ
وَاللهْ أَنْتُمْ مُرَادِي فِي الْدُّنَا وَالْقِيَامْ
Inu mwana wa Taha, mtima wanga watengeka ndi chikondi chanu
Pamaso pa Allah, inu ndinu chokhumba changa m’dziko lino ndi tsiku la chiukitsiro
وَمَا أَنَا إِلَّا بِكُمْ يَا سَادَتِي يَا كِرَامْ
عَلَيْكِ مَعَ وَالِدِكْ أَزْكَى الْصَّلَاةْ وَالسَّلَامْ
Ine ndilipo chifukwa cha inu nokha, inu atsogoleri anga owolowa manja
Pa inu pamodzi ndi atate anu pakhale madalitso ndi mtendere oyera kwambiri
وَأَهْلِ الْكِسَاءْ وَأَهْلِ بَيْتِهْ عَالِيِّينَ الْمَقَامْ
وَالْصَّحْبْ أَجْمَعْ وَمَنْ عَلَى هُدَاهْ اِسْتَقَامْ
Ndi anthu a m’mwinjiro ndi banja lake la maudindo apamwamba
Ndi masahaba onse ndi onse okhazikika pa chiongoko