لَمْ يَخْلُقِ الرَّحْمَنُ مِثْلَ مُحَمَّدٍ
Wachifundo sanalengepo wina wonga Muhammad
Ny
Ny
لَمْ يَخْلُقِ الرَّحْمَنُ مِثْلَ مُحَمَّدٍ
بَيْنَ الْوَرَى بَشَراً عَلَى الْإِطْلَاقِ
Wachifundo sanalengepo wina ofanana ndi Muhammad
pakati pa anthu onse m’zolengedwa zonse
كَلَّا وَلَا عَرَفَ الْخَلَائِقُ قَدْرَهُ
مَا فَوْقَهُ حَقّاً سِوَى الْخَلَّاقِ
Ayi, ndipo zolengedwa sizinazindikire ukulu wake;
palibe ali pamwamba pake ndithu kupatula Mulengi
مَاذَا أَقُولُ بِوَصْفِهِ وَمَدِيحِهِ
وَسَنَاهُ دَوْماً بَاهِرُ الْإِشْرَاقِ
Kodi ndinganene chiyani pomufotokoza ndi kumutamanda?
Pakuti kuwala kwake kumanyezimira modabwitsa nthawi zonse
وَهُوَ الَّذِي لِلْخَلْقِ أُرْسِلَ رَحْمَةً
وَأَتَى يُتَمِّمُ مَكَارِمَ الْأَخْلَاقِ
Iye ndiye amene anatumizidwa kukhala chifundo kwa zolengedwa,
ndipo anadza kudzatsiriza makhalidwe olemekezeka kwambiri