يَا أَجْمَلَ الْأَنْبِيَاء
Oh Most Beautiful of Prophets
Ny
يَا أَجْمَلَ الْأَنْبِيَاء
يَا أَكْمَلَ الْأَصْفِيَاء
Inu okongola koposa mwa aneneri
Inu angwiro koposa mwa osankhidwa
يَا خَاتَمَ الرُّسْلِ مَا
أَحْلَاكَ فِي قَلْبِي
Inu Chisindikizo cha Atumiki — m'mene
muliri okoma m'mtima mwanga!
يَا ذَا الَّذِي نُسْخَةُ
الْأَكْوَانِ فِيْكَ مَطْوِيَّ
Inu amene chithunzi cha
chilengedwe chili mwa inu chopindidwa
عَطِيَّةٌ أَزَلِيَّة
Mphatso yosatha komanso yamuyaya
أَنْتَ الَّذِي أُعْطِيتَ
الشَّفَاعَةَ الْوَافِيَّة
Inu ndinu amene munapatsidwa
Kupembedzera komaliza
وَ الْخَلْقُ حِينَئِذٍ
يَلْتَمِسُونَ الْأَنْبِيَاءْ
Ndipo pamene cholengedwa chonse
chikufunafuna aneneri
ثُمَّ يُقَالُ لِلْأَنَامْ
قَدْ نِلْتُمُ الْأُمْنِيَّة
Pamenepo anthu adzauzidwa:
"Mwachipeza chomwe mumachifuna—
أَلَا اقْصِدُوْا مُحَمَّدًا
بَابَ الْإِلَهِ الْعَالِيَ
Pitani kwa Muhammad,
Chipata cha Ambuye Wam'mwambamwamba."
آيَاتُهُ شَافِيَة
Zizindikiro zake ndi machiritso
وَهُوَ الْمُعَدُّ لَهَا
وَ ذُوَ الْثَنَاءِ الْوَافِيَ
Ndipo iye ndi wokonzekera zimenezi,
iye ndi mwini chitamando chokwanira
ثُمَّ يُنَادِي سَاجِدًا
يَا رَبِّ جُدْ رَاضِيَـا
Kenako adzafuula atagwada pansi:
"Inu Ambuye wanga, perekani ndipo mukhale okondwa!"
يُنَادِي اشْفَعْ يَا حَبِيْبِ
يَا صَفْوَةَ الْأَصْفِيَاءْ
Kudzanenedwa: "Pembedzerani, Inu Okondedwa!
Inu oyeretsedwa koposa mwa osankhidwa
وَسَلْ تُعْطَى مَا تَرُوْم
وَلَا تَدَعْ عَاصِيَا
Pemphani ndipo mudzapatsidwa,
ndipo musasiye wochimwa aliyense pambuyo."
يَا صَفْوَةَ الْأَصْفِيَاءْ
Inu oyeretsedwa koposa mwa osankhidwa
صَلُّوْا عَلَى مَنْ عَلَا
فَوْقَ السَّمَا رَاقِيَا
Perekani madalitso kwa Iye
Amene anakwera kupitirira kumwamba
هذَا حَبِيْبٌ غَدًا
عَنَّا العَنَـا مَـاحِيَا
Okondedwayu amene mawa
adzatichotsera masautso onse
يَا رَبَّنَا عَطَّفْ عَلَيْنَا
قَلْبَهُ الزَّاكِيَا
Inu Ambuye wathu, titembenuzireni
chifundo cha mtima wake woyera
وَاخْتِمْ لَنَا خِتَامَ مِسْكٍ
يَا مُجِيْبَ الدَّاعِيَا
Ndipo titsirizireni ndi fungo la miski,
Inu amene mumayankha opemphera
بِالْأَسْرَارِ الذَّاتِـيـــة
Ndi zinsinsi zakuya za Umulungu