هَذَا الْمَقَامُ الَّذِي لَاذَتْ بِهِ الْأُمَمُ
Malo awa omwe mitundu ya anthu idathawirako.
Ny
هَذَا الْمَقَامُ الَّذِي لَاذَتْ بِهِ الْأُمَمُ
وَأَذْعَنَتْ لِعُلَاهُ الْعُرْبُ وَالْعَجَمُ
Malo awa ndi omme mitundu ya anthu idathawirako
ndipo Aarabu ndi mitundu ina adagonjera ukulu wake
هَذَا مَقَامُ رَسُولِ اللَّهْ أَكْرَمُ مَنْ
جَاءَتْهُ مِنْ رَبِّهِ الْأَحْكَامُ وَالْحِكَمُ
Awa ndi malo a Mtumiki wa Allah, wolemekezeka kwambiri mwa onse
amene adalandira malamulo ndi nzeru kuchokera kwa Mbuye wake
هَذَا مُحَمَّدُ الْهَادِي الَّذِي مُحِيَتْ
عَنَّا بِنُورِ هُدَاهُ الْظُّلْمُ وَ الْظُّلَمُ
Uyu ndi Muhammad Mtsogoleri amene zidafufutidwa
kwa ife, ndi kuwala kwa chitsogozo chake, chizunzo ndi mdima
هَذَا الَّذِي قَدْ سَمَا فَوْقَ الْسَّمَا
إِلَى مَقَامِ عِزٍّ تَنَاهَتْ دُونَهُ الْأُمَمُ
Uyu ndi amene adakwera pamwamba pa thambo
kufika pamalo a ulemerero amene mitundu ina idalephera kufikako
يَا سَيِّدِي يَا رَسُولَ اللَّهْ يَا أَمَلِي
يَا مَنْ أَلُوذُ بِهِ إِنْ زَلَّتِ الْقَدَمُ
Inu mbuye wanga, inu Mtumiki wa Allah, inu chiyembekezo changa
inu amene ndidzakuthawirani ngati phazi langa litatelela
بِكَ اهْتَدَيْتُ إِلَى الْإِيمَانِ فَاتَّصَلَتْ
بِذَاكَ عِنْدِي مِنْ أَفْضَالِكَ الْنِّعَمُ
Kudzera mwa inu ndidatsogoleredwa ku chikhulupiriro
ndipo kudzera mu zimenezo, madalitso ochokera pa ulemu wanu adandifikira
صَلَّى عَلَيْكَ إِلَهُ الْخَلْقِ مَا سَجَعَتْ
وَرْقٌ وَمَا هَطَلَتْ مِنْ سُحْبِهَا دِيَمُ
Mulungu wa chilengedwe akudalitseni pamene mbalame zikuimba
ndiponso pamene mvula yosalekeza ikugwa kuchokera m’mitambo